9. Ndipo tsopano, mupepeze Mulungu, kuti aticitire cifundo; icico cicokera kwa inu; kodi Iye adzabvomereza ena a inu? ati Yehova wa makamu.
10. Mwenzi atakhala wina mwa inu wakutseka pamakomo, kuti musasonkhe moto cabe pa guwa langa la nsembe! Sindikondwera nanu, ati Yehova wa makamu, ndipo sindidzalandira capereka m'dzanja lanu.
11. Pakuti kuyambira koturukira dzuwa kufikira kolowera kwace dzina langa lidzakhala lalikuru mwa amitundu; ndipo m'malo monse adzaperekera dzina langa cofukiza ndi copereka coona; pakuti dzina langa lidzakhala lalikuru mwa amitundu, ati Yehova wa makamu.
12. Koma inu muliipsa, pakunena inu, Gome la Yehova laipsidwa, ndi zipatso zace, cakudya cace, conyozeka.
13. Mukutinso, Taonani, ncolemetsa ici! ndipo mwacipeputsa, ati Yehova wa makamu; ndipo mwabwera nazo zofunkha, ndi zotsimphina, ndi zodwala; momwemo mubwera nayo nsembe; kodi ndiyenera kuilandira ku dzanja lanu? ati Yehova.
14. Koma wotembereredwa wonyengayo, wokhala nayo yaimuna m'gulu lace, nawinda, naphera Yehova nsembe cinthu cacirema; pakuti Ine ndine mfumu yaikuru, ati Yehova wa makamu; ndipo dzina langa ndi loopsa pakati pa amitundu.