4. ndipo anagwa pansi, namva mau akunena naye, Saulo, Saulo, Undilondalonderanji?
5. Koma anati, Ndiouyani Mbuye? Ndipo anati, Ndine Yesu amene umlondalonda;
6. komatu, uka, nulowe m'mudzi, ndipo kudzanenedwa kwa iwe cimene uyenera kucita.
7. Ndipo amunawo akumperekeza iye anaima du, atamvadi mau, koma osaona munthu.
8. Ndipo Saulo anauka; koma potseguka maso ace, sanapenya kanthu; ndipo anamgwira dzanja, namtenga nalowa naye ni'Damasiko.
9. Ndipo anakhala masiku atatu wosaona, ndipo sanadya kapena kumwa.
10. Koma ku Damasiko kunali wophunzira wina dzina lace Hananiya; ndipo Ambuye anati kwa iye m'masomphenya, Hananiya. Ndipo anati, Ndiri pano, Ambuye,