Macitidwe 9:39-43 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

39. Ndipo Petro anayamuka, napita nao. M'mene anafikako, anapita naye ku cipinda ca pamwamba; ndipo amasiye onse anaimirirapo pali iye, nalira, namuonetsa maraya ndizobvala zimene Dorika adasoka, pamene anali nao pamodzi.

40. Koma Petro anawaturutsa onse, nagwada pansi, napemphera; ndipo potembenukira kumtembo anati, Tabita, uka. Ndipo anatsegula maso ace; ndipo pakuona Petro, anakhala tsonga.

41. Ndipo Petro anamgwiradzanja, namnyamutsa; ndipo m'mene adaitana oyera mtima ndi amasiye, anampereka iye wamoyo.

42. Ndipo kudadziwika ku Yopa konse: ndipo ambiri anakhulupirira Ambuye.

43. Ndipo kunali, kuti anakhala iye m'Yopa masiku ambiri ndi munthu Simoni wofufuta zikopa.

Macitidwe 9