Macitidwe 7:8-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndipo anaiupatsa iye cipangano ca mdulidwe; ndipo kotero Abrahamu anabala Isake, namdula tsiku lacisanu ndi citatu; ndi Isake anabala Yakobo, ndi Yakobo anabala makolo akulu aja khumi ndi awiri.

9. Ndipo makolo akuluwa podukidwa naye Yosefe, anamgulitsa amuke naye ku Aigupto; ndipo Mulungu anali naye,

10. namlanditsa iye m'zisautso zace zonse, nampatsa cisomo ndi nzeru pamaso pa Farao mfumu ya ku Aigupto; ndipo anamuika iye kazembe wa pa Aigupto ndi pa nyumba yace yonse.

11. Koma inadza njala pa Aigupto ndi Kanani lonse, ndi cisautso cacikuru; ndipo sanapeza cakudya makolo athu.

12. Koma pakumva Yakobo kuti muli tirigu m'Aigupto, anatuma makolo athu ulendo woyamba,

Macitidwe 7