3. Cifukwa cace, abale, yang'anani mwa inu amuna asanu ndi awiri a mbiri yahwino, odzala ndi Mzimu ndi nzeru, amene tikawaike asunge nchito iyi.
4. Koma ife tidzalimbika m'kupemphera, ndi kutumikira mau.
5. Ndipo mau amene anakonda unyinji wonse; ndipo anasankha Stefano, ndiye munthu wodzala ndi cikhulupiriro ndi Mzimu Woyera, ndi Filipo, ndi Prokoro, ndi Nikanora ndi Timo, ndi Parmena, ndi Nikolao, ndiye wopinduka wa ku Antiokeya:
6. amenewo anawaika pamasopa atumwi; ndipo m'mene adapemphera, anaika manja pa iwo.