23. Ndipo m'mene anamasulidwa, anadza kwa anzao a iwo okha, nawauza ziri zonse oweruza ndi akulu adanena nao.
24. Ndipo m'mene adamva, anakweza mau kwa Mulungu ndi mtima umodzi, nati, Mfumu, Inu ndinu wolenga thambo la kumwamba ndi dziko, ndi nyanja, ndi zonse ziri m'menemo;
25. amene mwa Mzimu Woyera, pakamwa pa kholo lathu Davine mtumiki wanu, mudati,Amitundu anasokosera cifukwaciani?Nalingirira zopanda pace anthu?
26. Anadzindandalitsa mafumu a dziko,Ndipo oweruza anasonkhanidwa pamodzi,Kutsutsana ndi Ambuye, ndi Kristu wace.