17. Komatu tiwaopse asalankhulenso m'dzina ili kwa munthu ali yense, kuti cisabukenso kwa anthu.
18. Ndipo anawaitana, nawalamulira kuti asanene konse kapena kuphunzitsa m'dzina la Yesu.
19. Koma Petro ndi Yohane anayankha nati kwa iwo, Weruzani, ngati nkwabwino pamaso pa Mulungu kumvera inu koposa Mulungu;
20. pakuti sitingatheife kuleka kulankhula zimene tinaziona ndi kuzimva.
21. Koma m'mene anawaopsanso anawamasula, osapeza kanthu kakuwalanga, cifukwa ca anthu; pakuti onse analemekeza Mulungu cifukwa ca comwe cidacitika.