Macitidwe 25:25-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. Koma ndinapeza ine kuti sanacita kanthu, koyenera imfa iye; ndipo popeza, iye yekha anati akaturukire kwa Augusto, ndatsimikiza mtima kumtumizako.

26. Koma ndiribe ine kanthu koti ndinenetse za iye kakulembera kwa mbuye wanga. Cifukwa cace ndamturutsira kwa inu, ndipo makamaka kwa inu, Mfumu Agripa, kuti, ndikatha kumfunsafunsa, ndikhale nako kanthu kakulembera.

27. Pakuti cindionekera copanda nzeru, potumiza wam'nsinga, wosachulanso zifukwa zoti amneneze.

Macitidwe 25