1. Pamenepo Festo m'mene analowa dziko lace, ndipo atapita masiku atatu, anakwera kunka ku Yerusalemu kucokera ku Kaisareya.
2. Ndipo ansembe akulu ndi akulu a Ayuda ananenera Paulo kwa iye; ndipo iwo anamdandaulira,
3. nampempha kuti mlandu wace wa Paulo uipe, kuti amuitane iye adze ku Yerusalemu; iwo amcitira cifwamba kuti amuphe panjira.
4. Pamenepo Festo anayankha, kuti Paulo asungike ku Kaisareya, ndi kuti iye mwini adzapitako posacedwa.