Macitidwe 24:8-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. kwa iye mudzakhoza kuzindikira pomfunsa nokha, za izi zonse timnenerazi.

9. Ndipo Ayudanso anabvomerezana naye, natsimikiza kuti izi zitero.

10. Ndipo pamene kazembe anamkodola kuti anene, Paulo anayankha, Podziwa ine kuti mwakhala woweruza wa mtundu uwu zaka zambiri, ndidzikanira mokondwera;

11. popeza mukhoza kuzindikira kuti apita masiku khumi ndi awiri okha cikwerere ine ku Yerusalemu kukalambira;

12. ndipo sanandipeza m'Kacisi wotsutsana ndi munthu, kapena kuutsa khamu la anthu, kapena m'sunagoge kapena m'mzinda.

Macitidwe 24