Macitidwe 24:17-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Ndipo zitapita zaka zambiri ndinadza kutengera mtundu wanga zacifundo, ndi zopereka;

18. popereka izi anandipeza woyeretsedwa m'Kacisi, wopanda khamu la anthu, kapena phokoso; koma panali Ayuda ena a ku Asiya,

19. ndiwo mwenzi atakhala pano pamaso panu ndi kundinenera, ngati ali nako kanthu kotsutsa ine.

20. Kapena iwo amene ali kunowa anene anapeza cosalungama cotani, poimirira ine pamaso pa bwalo la akuru,

Macitidwe 24