9. Ndipo munthuyu anali nao ana akazi anai, anamwali, amene ananenera.
10. Ndipo pokhalapo masiku ambiri, anatsika ku Yudeya mneneri, dzina lace Agabo.
11. Ndipo anadza kwa ife natenga lamba la Paulo, nadzimanga yekha manja ndi mapazi, nati, Atero Mzimu Woyera, Munthu mwini lamba ili, adzammanga kotero Ayuda a m'Yerusalemu, nadzampereka m'manja a amitundu.
12. Koma pamene tinamva izi tinamdandaulira ife ndi iwo a komweko, asakwere iye kunka ku Yerusalemu.