33. Pamenepo poyandikira kapitao wamkuru anamgwira iye, nalamulira ammange ndi maunyolo awir; ndipo anafunsira, ndiye yani, ndipo anacita ciani?
34. Koma wina anapfuula kena, wina kena, m'khamumo; ndipo m'mene sanathe kudziwa zoona cifukwa ca phokosolo analamulira amuke naye kulinga.
35. Ndipo pamene anafika pamakwerero, kudatero kuti anamsenza asilikari cifukwa ca kulimbalimba kwa khamulo;
36. pakuti unyinji wa anthu unatsata, nupfuula, Mcotse iye.