Macitidwe 20:4-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndipo anamperekeza kufikira ku Asiya Sopatro mwana wa Puro, wa ku Bereya; ndipo Atesalonika, Aristarko ndi Sekundo; ndi Gayo wa ku Derbe, ndi Timoteo; ndi a ku Asiya, Tukiko ndi Trofimo.

5. Koma iwowa adatitsogolera, natilinda ku Trowa.

6. Ndipo tinapita m'ngalawa kucokera ku Filipi, atapita masiku a mkate wopanda cotupitsa, ndipo popita masiku asanu tinawapeza ku Trowa; pamenepo tinatsotsa masiku asanu ndi awiri.

7. Ndipo tsiku loyamba la sabata, posonkhana ife kunyema mkate, Paulo anawafotokozera mau, popeza anati acoke m'mawa mwace; ndipo ananena cinenere kufikira pakati pa usiku.

8. Ndipo munali nyali zambiri m'cipinda ca pamwamba m'mene tinasonkhanamo.

9. Ndipo mnyamata dzina lace Utiko anakhala pazenera, wogwidwa nato tulo tatikuru; ndipo pakukhala cifotokozere Paulo, ndipo pogwidwa nato tulo, anagwa posanja paciwiri, ndipo anamtola wakufa.

10. Ndipo potsikirako Paulo, anamgwera namfungatira, nati, Musacite phokoso, pakuti moyo wace ulipo.

Macitidwe 20