7. Ndipo anadabwa onse, nazizwa, nanena, Taonani, awa onse alankhulawa sali Agalileya kodi?
8. ndipo nanga ife timva bwanji, yense m'cilankhulidwe cathu cimene tinabadwa naco?
9. Aparti ndi Amedi, ndi Aelami, ndi iwo akukhala m'Mesopotamiya, m'Yudeya, ndiponso m'Kapadokiya, m'Ponto, ndi m'Asiya;
10. m'Frugiya, ndiponso m'Pamfuliya, m'Aigupto, ndi mbali za Libiya wa ku Kurene, ndi alendo ocokera ku Roma, ndiwo Ayuda, ndiponso opinduka,
11. Akrete, ndi Aarabu, tiwamva iwo alikulankhula m'malilime athu zazikuru za Mulungu.
12. Ndipo anadabwa onse, nathedwa nzeru, nanena wina ndi mnzace, Kodi ici nciani?