Macitidwe 2:46-47 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

46. Ndipo tsiku ndi tsiku 7 anali cikhalire ndi mtima umodzi m'Kacisi, ndipo ananyema mkate kunyumba kwao, nalandira cakudya ndi msangalalo, ndi mtima woona;

47. nalemekeza Mulungu, 8 ndi kukhala naco cisomo ndi anthu onse. Ndipo 9 Ambuye anawaonjezera tsiku ndi tsiku amene akuti apulumutsidwe.

Macitidwe 2