Macitidwe 19:38-41 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

38. Ngati tsono Demetriyo ndi amisiri okhala naye, ali ndi mlandu ndi munthu, mabwalo a mirandu alipo, ndi ziwanga ziripo; anenezane.

39. Koma ngati mufuna kanthu ka zinthu zina, kadzakonzeka m'msonkhano wolamulidwa.

40. Pakutinso palipo potiopsya kuti adzatineneza za cipolowe ca lero; popeza palibe cifukwa ca kufotokozera za cipiringu cimene.

41. Ndipo pamene ananena izi, anamasula msonkhano.

Macitidwe 19