Macitidwe 18:9-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndipo Ambuye anati kwa Paulo usiku m'masomphenya, Usaope, koma nena, usakhale cete;

10. cifukwa Ine ndiri pamodzi ndi iwe, ndipo palibe munthu adzautsana ndi iwe kuti akuipse; cifukwa ndiri nao anthu ambiri m'mudzi muno.

11. Ndipo anakhala komwe caka cimodzi kudza miyezi isanu ndi umodzi; naphunzitsamau a Mulungu mwa iwo.

12. Tsono pamene Galiyo anali ciwanga ca Akaya, Ayuda ndi mtima umodzi anamuukira Paulo, nanka naye ku mpando wa ciweruziro,

Macitidwe 18