Macitidwe 14:20-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Koma pamene, anamzinga akuphunzirawo, anauka iye, nalowa m'mudzi; m'mawa mwace anaturuka ndi Bamaba kunka, ku Derbe.

21. Pamene analalikira Uthenga Wabwino pamudzipo, nayesa ambiri akuphunzira, anabwera ku Lustra ndi Ikoniyo ndi Antiokeya,

22. nalimbikitsa mitima ya akuphunzira, nadandauliraiwo kuti akhalebe m'cikhulupiriro, ndi kuti tiyenera kulowa m'ufumu wa Mulungu ndi zisautso zambiri.

23. Ndipo pamene anawaikira akuru mosankha mu Mpingo Mpingo, ndi kupemphera pamodzi ndi kusala kudya, anaikiza iwo kwa Ambuye amene anamkhulupirirayo.

24. Ndipo anapitirira pa Pisidiya, nafika ku Pamfuliya.

25. Ndipo atalankhula mau m'Perge, anatsikira ku Ataliya;

Macitidwe 14