Macitidwe 12:23-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. Ndipo pomwepo mngelo wa Ambuye anamkantha, cifukwa sanampatsa Mulungu ulemerero; ndipo anadyedwa ndi mphutsi, natsirizika.

24. Koma mau a Mulungu anakula, nacurukitsa.

25. Ndipo Bamaba ndi Saulo anabwera kucokera ku Yerusalemu m'mene adatsiriza utumiki wao, natenga Yohane wonenedwanso Marko amuke nao.

Macitidwe 12