20. Koma Herode anaipidwa nao a ku Turo ndi Sidoni; ndipo anamdzera iye ndi mtima umodzi, ndipo m'mene adakopa Blasto mdindo wa mfumu, anapempha mtendere, popeza dziko lao linapeza zakudya zocokera ku dziko la mfumu.
21. Ndipo tsiku lopangira Herode anabvala zobvala zacifumu, nakhala pa mpando wacifumu, nawafotokozera iwo mau a pabwalo.
22. Ndipo anthu osonkhanidwawo anapfuula, Ndiwo mau a Mulungu, si a munthu ai.