Macitidwe 11:5-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Ndinali ine m'mudzi wa Yopa ndi kupemphera; ndipo m'kukomoka ndinaona masomphenya, cotengera cirikutsika, ngati cinsaru cacikuru cogwiridwa pa ngondya zace zinai; ndi kutsika kumwamba, ndipo cinadza pali ine;

6. cimeneco ndidacipenyetsetsa ndinacilingirira, ndipo ndinaona nyama za miyendo inai za padziko ndi zirombo, ndi zokwawa, ndi mbalame za m'mlengalenga.

7. Ndipo ndinamvanso mau akunena ndi ine, Tauka Petro; ipha, nudye.

8. Koma ndinati, Iaitu, Ambuye; pakuti kanthu wamba, kapena konyansa sikanalowe m'kamwa mwanga ndi kale lonse.

9. Koma mau anayankha nthawi yaciwiri oturuka m'mwamba, Cimene Mulungu anaciyeretsa, usaciyesera cinthu wamba.

10. Ndipo ici cinacitika katatu; ndipo zinakwezekanso zonse kumwamba.

11. Ndipo taonani, pomwepo amuna atatu anaima pa khomo la nyumba m'mene munali ife, anatumidwa kwa ine ocokera ku Kaisareya.

Macitidwe 11