39. Ndipo ife ndife mboni zazonse adazicita m'dzikola Ayuda ndim'Yerusalemu; amenenso anamupha, nampacika pamtengo,
40. Ameneyo, Mulungu anamuukitsa tsiku lacitatu, nalola kuti aonetsedwe,
41. si kwa anthu onse ai, koma kwa mboni zosankhidwiratu ndi Mulungu, 1 ndiwo ife amene tinadya ndi kumwa naye pamodzi, atauka iye kwa akufa.
42. Ndipo 2 anatilamulira ife tilalikire kwa anthu, ndipo ticite umboni kuti 3 Uyu ndiye amene aikidwa ndi Mulungu akhale woweruza amoyo ndi akufa.
43. 4 Ameneyu aneneri onse amcitira umboni, kuti onse akumkhulupirira iye adzalandira cikhululukiro ca macimo ao, mwa dzina lace.