12. m'menemo munali nyama za miyendo inai za mitundu yonse, ndi zokwawa za padziko ndi mbalame za m'mlengalenga.
13. Ndipo anamdzera mau, Tauka, Petro; ipha, nudye.
14. Koma Petro anati, Iaitu, Mbuye; pakuti sindinadya ine ndi kale lonse kanthu wamba ndi konyansa.
15. Ndipo mau anamdzeranso nthawi yaciwiri, Cimene Mulungu anayeretsa, usaciyesa cinthu wamba.
16. Ndipo cinacitika katatu ici; ndipo pomwepo cotengeraco cinatengedwa kunka kumwamba.
17. Ndipo pokayika-kayika Petro mwa yekha ndi kuti masomphenya adawaona akuti ciani, taonani, amuna aja otumidwa ndi Komeliyo, atafunsira nyumba ya Simoni, anaima pa cipata,