17. Cifukwa anali wowerengedwa mwa ife, ndipo analandira gawo lace la utumiki uwu.
18. (Uyutu tsono anadzitengera kadziko ndi mphoto ya cosalungama; ndipo anagwa camutu, naphulika pakati, ndi matumbo ace onse anakhuthuka;
19. ndipo cinadziwika ndi onse akukhala ku Yerusalemu; kotero kuti m'manenedwe ao kadzikoka kanachedwa Akeldama, ndiko, kadziko ka mwazi.)
20. Pakuti kwalembedwa m'buku la Masalmo,Pogonera pace pakhale bwinja,Ndipo pasakhale munthu wogonapo;Ndipo uyang'aniro wace autenge wina.
21. Potero kuyenera kuti wina wa amunawo anatsatana nafe nthawi yonseyi Ambuye Yesu analowa naturuka mwa ife,