15. Ndipo m'masiku awa anaimirira Petro pakati pa abale, nati (gulu la anthu losonkhana pamalo pomwe ndilo ngati zana limodzi ndi makumi awiri),
16. Amuna inu, abale, kunayenera kuti lemba likwanitsidwe, limene Mzimu Woyera anayamba kunena mwa m'kamwa mwa Davine za Yudase, wokhala mtsogoleri wa iwo adagwira Yesu.
17. Cifukwa anali wowerengedwa mwa ife, ndipo analandira gawo lace la utumiki uwu.
18. (Uyutu tsono anadzitengera kadziko ndi mphoto ya cosalungama; ndipo anagwa camutu, naphulika pakati, ndi matumbo ace onse anakhuthuka;