9. Ndipo Iyeananyamuka, naimirira. Ndipo Yesuanati kwa iwo, Ndikufunsani inu, Kodi nkulola tsiku la Sabata, kucita zabwino, kapena kucita zoipa? kupulumutsa moyo, kapena kuuononga?
10. Ndipo pamene anaunguza-unguza pa iwo onse, anati kwa iye, Tansa dzanja lako, Ndipo iye anatero, ndi dzanja lace lina; bwerera momwe.
11. Koma iwowo anagwidwa misala; nalankhulana wina ndi mnzace kuti amcitire Yesu ciani.
12. Ndipo kunali masiku awa, iye anaturuka nanka kuphiri kukapemphera; nacezera usiku wonse m'kupemphera kwa Mulungu.
13. Ndipo kutaca, anaitana ophunzira ace; nasankha mwa iwo khumi ndi awiri, amene anawachanso dzina lao atumwi: