30. Koma iye anapyola pakati pao, nacokapo.
31. Ndipo iye anatsika nadza ku Kapernao, ndiwo mudzi wa ku Galileya, Ndipo analikuwaphunzitsa iwo pa Sabata; ndipo anadabwa ndi ciphunzitso cace;
32. cifukwa mau ace anali ndi ulamuliro.
33. Ndipo munali m'sunagoge munthu, wokhala naco ciwanda conyansa; napfuula ndi mau olimba, kuti,
34. Ha! tiri ndi ciani ndi Inu, Yesu wa ku N azarete? kodi munadza kutiononga ife? ndikudziwani Inu muli yani, ndinu Woyera wace wa Mulungu.