Luka 4:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yesu, wodzala ndi Mzimu Woyera, anabwera kucokera ku Yordano, natsogozedwa ndi Mzimu kunka kucipululu kukayesedwa ndi mdierekezi masiku makumi anai.

2. Ndipo iye sanadya kanthu masiku awo; ndipo pamene anatha anamva njala.

3. Ndipo mdierekezi anati kwa iye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, uzani mwala uwu usanduke mkate.

4. Ndipo Yesu anayankha nati kwa iye, Kwalembedwa, kuti,Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha.

Luka 4