1. Ndipo Yesu, wodzala ndi Mzimu Woyera, anabwera kucokera ku Yordano, natsogozedwa ndi Mzimu kunka kucipululu kukayesedwa ndi mdierekezi masiku makumi anai.
2. Ndipo iye sanadya kanthu masiku awo; ndipo pamene anatha anamva njala.
3. Ndipo mdierekezi anati kwa iye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, uzani mwala uwu usanduke mkate.