3. Ndipo m'mene analowa sanapeza mtembo wa Ambuye Yesu.
4. Ndipo kunali, m'mene anathedwa nzeru naco, taonani amuna awiri anaimirira pafupi pao atabvala zonyezimira;
5. ndipo m'mene anakhala ndi mantha naweramira pansi nkhope zao, anati kwa iwo, Mufuniranji wamoyo pa akufa?
6. Palibe kuno iye, komatu anauka; kumbukilani muja adalankhula nanu, pamene analinso m'Galileya,
7. ndi kunena, kuti, Mwana wa munthu ayenera kuperekedwa m'manja a anthu ocimwa, ndi kupacikidwa pamtanda, ndi kuuka tsiku lacitatu.