Luka 23:38-40 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

38. Ndipo kunalinso lembo pamwamba pace, ndilo: UYU NDIYE MFUMU YAAYUDA.

39. Ndipo mmodzi wa ocita zoipa anapacikidwawo anamcitira iye mwano nanena, Kodi suli Kristu Iwe? udzipulumutse wekha ndi ife.

40. Koma winayo anayankha, namdzudzula iye, nati, Kodi suopa Mulungu, poona uli m'kulangika komweku?

Luka 23