1. Ndipo khamu lonselo Iinanyamuka kupita naye kwa Pilato.
2. Ndipo anayamba kumnenera iye, kuti, Tinapeza munthu uyu alikupandutsa anthu a mtundu wathu, ndi kuwaletsa kupereka msonkho kwa Kaisara, nadzinenera kuti iye yekha ndiye Kristu mfumu.
3. Ndipo Pilato anamfunsa iye, nanena, Kodindiwe mfumu ya Ayuda? Ndipo iye anamyankha nati, Mwatero.