29. ndipo Ine ndikuikirani ufumu, monganso Atate wanga anandiikira Ine, kuti mukadye ndi kumwa kugome kwanga mu Ufumu wanga;
30. ndipo mudzakhala pa mipando yacifumu ndi kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israyeli.
31. Simoni, Simoni, taona, Satana anafunsa akutengeni kuti akupeteni ngati tirigu;
32. koma ndinakupempherera kuti cikhulupiriro cako cingazime; ndipo iwe, pamene watembenuka ukhazikitse abale ako.
33. Ndipo anati kwa iye, Ambuye, ndiripo ndikapite ndi Inu kundende ndikuimfa.