28. Komapoyamba kucitika izi weramukani, tukulani mitu yanu; cifukwa ciomboledwe canu cayandikira.
29. Ndipo ananena nao fanizo; Onani mkuyu, ndi mitengo yonse:
30. pamene iphukira, muipenya nimuzindikira pa nokha kuti dzinja liri pafupi pomwepo.
31. Inde cotero inunso, pakuona zinthu izi zirikucitika, zindikirani kuti Ufumu wa Mulungu uli pafupi.
32. Indetu ndinena ndinu, Mbadwo uno sudzapitirira, kufikira zonse zitacitika.
33. Kumwamba ndi dziko lapansi zidzapita; koma mau anga sadzapita.