Luka 19:28-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. Ndipo m'mene adanena izi anawatsogolera nakwera ku Yerusalemu.

29. Ndipo kunali, m'mene anayandikira ku Betefage ndi Betaniya, pa phiri lochedwa la Azitona, anatuma awiri a ophunzira,

30. nati, Mukani ku mudzi uli pandunji panu; m'menemo, polowa, mudzapeza mwana wa buru womangidwa, pamenepo palibe munthu anakwerapo nthawi iri yonse; mummasule iye nimumtenge.

Luka 19