32. Pakuti adzampereka kwa amitundu, nadzamseka, nadzamcitira cipongwe, nadzamthira malobvu; ndipo atamkwapula adzamupha iye;
33. ndipo tsiku lacitatu adzauka.
34. Ndipo sanadziwitsa kanthu ka izi; ndi mau awa adawabisikira, ndipo sanazindikira zonenedwazo.
35. Ndipo kunali, pamene anayandikira ku Yeriko, msaona wina anakhala m'mbali mwa njira, napemphapempha;
36. ndipo pakumva khamu la anthu alinkupita, anafunsa, ici nciani?
37. Ndipo anamuuza iye, kuti, Yesu Mnazarayo alinkupita.
38. Ndipo anapfuula, nanena, Yesu, Mwana wa Davine, mundicitire cifundo.