Luka 17:23-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. Ndipo adzanena ndi inu, Taonani ilo! taonani ili! musacoka kapena kuwatsata;

24. pakuti monga mphezi ing'anipa kucokera kwina pansi pa thambo, niunikira kufikira kwina pansi pa thambo, kotero adzakhala Mwana wa munthu m'tsiku lace.

25. Koma ayenera athange wamva zowawa zambiri nakanizidwe ndi mbadwo uno.

Luka 17