2. Koma kulibe kanthu kobvundikiridwa kamene sikadzaululidwa; ndi kobisika kamene sikadzadziwika.
3. Cifukwa cace zonse zimene mwazinena mumdima zidzamveka poyera; ndipo cimene mwalankhula m'khutu, m'zipinda za m'kati cidzalalikidwa pa macindwi a nyumba.
4. Ndipo ndinena kwa inu, abwenzi anga, Musaope iwo akupha thupi, ndipo akatha ici alibe kanthu kena angathe kucita.
5. Koma ndidzakulangizani amene muzimuopa; taopani iye amene atatha kupha ali ndi mphamvu yakutaya kugehena, inde, ndinena ndinu opani ameneyo.
6. Kodi mpheta zisanu sizigulidwa timakobiri tiwiri? ndipo palibe imodzi ya izo iiwalika pamaso pa Mulungu;