65. Ndipo panagwa mantha pa iwo onse akukhala oyandikana nao; ndipo analankhulalankhula nkhani izi zonse m'dziko: lonse la mapiri a Yudeya,
66. Ndipo onse amene anazimva anazisunga m'mtima mwao, nanena, Nangamwana uyu adzakhala wotani? Pakuti 13 dzanja la Ambuye linakhala pamodzi ndi iye.
67. Ndipo atate wace Zakariya anadzazidwa ndi Mzimu Woyera, nanenera za Mulungu, nati,
68. Wolemekezeka Ambuye, Mulungu wa Israyeli;14 Cifukwa iye anayang'ana, nacitira anthu ace ciombolo,