Luka 1:35-39 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

35. Ndipo mngelo anayankha, nati kwa iye, Mzimu Woyera adzafika pa iwe, ndi mphamvu ya Wamkulukulu idzakuphimba iwe: cifukwa cacenso Coyeraco cikadzabadwa, cidzachedwa Mwana wa Mulungu.

36. Ndipo taona, Elisabeti mbale wako, iyenso ali ndi pakati pa mwana wamwamuna m'ukalamba wace; ndipo mwezi uno uli wacisanu ndi cimodzi wa iye amene ananenedwa wouma.

37. Cifukwa 1 palibe mau amodzi akucokera kwa Mulungu adzakhala opanda mphamvu.

38. Ndipo Mariya anati, Onani, mdzakazi wa Ambuye; kukhale kwa ine monga mwa mau anu. Ndipo mngelo anacoka kwa iye.

39. Ndipo Mariya ananyamuka masiku amenewa, namuka ndi cangu ku dziko la mapiri ku mudzi wa Yuda;

Luka 1