Levitiko 4:35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

nawacotse mafuta ace onse, monga umo amacotsera mafuta a nkhosa pa nsembe yoyamika; ndipo wansembeyo atenthe, awa pa guwa la nsembe, monga umo amacitira nsembe zamoto za Yehova; ndipo wansembeyo amcitire comtetezera pa kucimwa kwace adakucimwira, ndipo adzakhululukidwa.

Levitiko 4

Levitiko 4:25-35