Levitiko 4:19-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Ndipo acotse mafuta ace onse, nawatenthe pa guwa la nsembe.

20. Atero nayo ng'ombeyo; monga umo anacitira ng'ombe ya nsembe yaucimo; ndipo wansembe awacitire cowatetezera, ndipo adzakhululukidwa.

21. Ndipo aturutse ng'ombeyo kunja kwa cigono, ndi kuitentha monga anatenthera ng'ombe yoyamba ija; ndiyo nsembe yaucimo ya kwa msonkhano.

22. Akacimwa mkuru, osati dala, pa cina ca zinthu ziti zonse aziletsa Yehova Mulungu wace, naparamula;

23. akamdziwitsa kucimwa kwace adacimwako, azidza naco copereka cace, ndico tonde wopanda cirema;

Levitiko 4