15. ndi imso ziwiri, ndi mafuta ali pomwepo, okhala m'cuuno, ndi cokuta ca mphafa cofikira kuimso.
16. Ndipo wansembe atenthe izi pa guwa la nsembe; ndizo cakudya ca nsembe yamoto icite pfungo lokoma; mafuta onse nga Yehova.
17. Likhale lemba losatha m'mibadwo yanu m'nyumba zanu zonse, musamadya kapena mafuta kapena mwazi.