1. Ndipo copereka cace cikakhala nsembe yoyamika; akabwera nayo ng'ombe, kapena yaimuna kapena yaikazi, azibwera nayo yopanda cirema pamaso pa Yehova.
2. Ndipo aike dzanja lace pa mutu wa copereka cace, ndi kuipha pa cipata ca cihema cokomanako; ndipo ana a Aroni, ansembewo, awaze mwazi wace pa guwa la nsembe pozungulira.