15. ndipo mukakaniza malemba anga, ndi moyo wanu ukanyansidwa nao maweruzo anga, kotero kuti simudzacita malamulo anga onse, koma kutyola cipangano canga;
16. ndidzacitira inu icinso; ndidzakuikirani zoopsa, nthendayoondetsayam'cifuwa ndi malungo, zakulanda maso ndi mphamvu, ndi kuzunza moyo; ndipo mudzabzala mbeu zanu cabe, pope za adani anu adzazidya.
17. Ndipt nkhope yanga idzatsutsana nanu kuti adani anu adzakukanthani, ndipt akudana ndi inu adzacita ufumu Pl inu ndipo mudzathawa wopanda wakukulondolani.
18. Ndipo muka panda kundimvera, zingakhale izi ndidzaonjeza kukulangani kasanu nd kawiri cifukwa ca zocimwa zanu.