1. Ndipo munthu akabwera naco copereka ndico nsembe yaufa ya kwa Yehova, copereka cace cizikhala ca ufa wosalala; ndipo athirepo mafuta, ndi kuikapo libano.
2. Ndipo abwere nayo kwa ana a Aroni, ansembewo; natengeko ufa, ndi mafuta odzala manja, ndi libano wace wonse; ndipo wansembeyo aitenthe cikumbutso cace pa guwa la nsembe, ndiyo nsembe yamoto, ya pfungo lokoma la kwa Yehova.
3. Ndipo cotsalira ca nsembe yaufa cikhale ca Aroni ndi ana ace; ndico copatulikitsa ca nsembe zamoto za Yehova.