Levitiko 19:6-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Tsiku lomwelo mwaipha, ndi m'mawa mwace muidye; ngati katsalirako kanthu tsiku lacitatu, muzikatentha ndi moto.

7. Akakadya konse tsiku tacitatu kali conyansa, kosabvomerezeka:

8. koma ali yense akudyako adzasenza mphulupulu yace, popeza waipsa copatulidwa ca Yehova; ndi munthuyo amsadze, kumcotsa kwa anthu a mtundu wace.

Levitiko 19