Levitiko 16:24-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Ndipo asambe thupi lace ndi madzi kumalo kopatulika, nabvale zobvala zace, naturuke, napereke nsembe yopsereza yace, ndi nsembe yopsereza ya anthu, nacite codzitetezera yekha ndi anthu.

25. Ndipo atenthe mafuta a nsembe yaucimo pa guwa la nsembe.

26. Ndipo iye amene anacotsa mbuzi ipite kwa Azazeli atsuke zobvala zace, nasambe thupi lace ndi madzi, ndipo atatero alowenso kucigono.

27. Koma ng'ombe ya nsembe yaucimo, ndi mbuzi ya nsembe yaucimo, zimene mwazi wao analowa nao kucita nao cotetezera m'malo opatulika, aturuke nazo kunja kwa cigono; natenthe ndi mota zikopa zao, ndi nyama zao, ndi cipwidza cao.

28. Ndi iye amene anazitentha atsuke zobvala zace, nasambe thupi lace ndi madzi, ndipo atatero alowenso kucigono.

Levitiko 16