1. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, atamwalira ana amuna awiri a Aroni, muja anasendera pamaso pa Yehova, namwalira;
2. ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni mbale wako, kuti asalowe nthawi zonse m'malo opatulika m'tseri mwa nsaru yocinga, pali cotetezerapo cokhala palikasa, kuti angafe; popeza ndioneka mumtambo pacotetezerapo.